Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Khulubvi Arts and Cultural Festival yafika pa mpondachimera

Phwando lolimbikitsa luso ndi chikhalidwe lodziwika kuti Khulubvi Arts and Cultural Festival, lomwe layamba dzulo lachisanu pa 28 June ndipo litha mawa pa 30 June 2024, linafika pachimake lero loweruka pa bwalo la Nsanje Prison m’boma la Nsanje. 

Mwazina, magule amakolo achikhalidwe chachi Sena, zakudya zawo komanso luso losiyanasiyana kuphatikizapo kuimba, ndi zina zomwe zikukometsera phwandoli.

Malinga ndi m’modzi mwa amene amayendetsa phwandoli, a Eric Trinta, iyi ndi njira imodzi yobweretsa pamodzi anthu aku chigwa cha mtsinje wa Shire kuti akumbutsane mbiri yawo posunga miyambo ndi chikhalidwe.

“Tikufuna kuti aMalawi adziwe kuti kuno ku chigwa cha Shire kulinso zabwino zambiri kuphatikizapo chikhalidwe chathu zomwe zingathandizire kuti chuma cha dziko lino chikwere kudzera muzokopa alendo komanso luso losiyanasiyana lomwe anthu akuno alinalo,” a Trinta anauza MBC Digital.

Iwo anatinso zokonzekera zonse zili m’chimake pofuna kukhadzikitsa gulu la Sena Cultural Heritage lomwe lidzisunga mbiri ndi chikhalidwe cha a Sena.

Ena mwa alendo olemekezeka omwe afika pa phwandoli ndi bwanankubwa wa boma la Nsanje, a Dominic Mwandira komanso a Senior Chief Chimombo.

Chaka chino ndi chachinayi chiyambireni phwando lolimbikitsa luso ndi chikhalidwe la Khulubvi Arts and Cultural Festival.

 

Olemba : McAllan Mapinda

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Osewera watsopano wa Wanderers Tanjong apezeka kumathero asabatayi

MBC Online

GOOD PROGRESS IN RESTORING PUBLIC SERVICE DELIVERY – CHAKWERA

Secret Segula

MW TO ENGAGE ANGOLA ON ENERGY

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.