Timu ya Silver Strikers idakali patsogolo pa m’ndandanda wa matimu amu TNM Super League itagonjetsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets 1-0 Lamulungu pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.
Silver Strikers inagoletsa kudzera mwa Chinsinsi Maonga, amene anamwetsa pa mphindi 90, atangoonjezera mphindi zisanu.
Maonga adagoletsa patangodutsa mphindi imodzi yokha atalowa, kusinthana ndi Binwell Katinji, kuti akateteze pamene timu ya Bullets imasewera corner.
Otchinga kumbuyo a Silver atachotsapo mpira n’kupita nawo kutsogolo, Patrick Macheso anamponyera Maonga yemwe anapezekapo aliyekha ndipo sanachedwetse koma kugoletsa.
Posangalala, iye anathamangira kumene kuli mbendera yakumanzere ndipo anachita kuvula mayala ndikuyenda ngati wadzitho, kupangitsa kuti oyimbila Gift Chicco amupatse khadi ya chikasu.
Ochemelera ambiri a Bullets anayamba kutuluka ndipo panthawi yomweyi, masewerowa anayima kaye chifukwa anthu ena ochemelera anayamba kugenda m’bwalo la masewero, ngakhale sizinaoneke kuti amagenda ndani komanso chifukwa chani.
Ndipo patadutsa mphundi khumi anathetsa masewerowa.
Otchinga pa golo wa timu ya Silver Strikers, George Chikooka, ndiye anamupatsa mphoto ngati ya osewera wapamwamba m’masewerowa.
Mphunzitsi wa timuyi, a Peter Mponda, anati chigoli cha Maonga chinali chovuta komanso anayamikira osewera ake akumbuyo pogwira ntchito yodalilika.
Wachiwiri kwa mphunzitsi wa timu ya Bullets, a Heston Munthali, anati iwo samayembekezera kuti agonja popeza anapeza mipata ya mbiri yomwe sanagwiritsire ntchito ndipo anati apanga zothekera kuti akonze vutoli.
Mbali inayi, timu ya Bangwe All Stars yathambitsa Chitipa United ndi zigoli zitatu kwa duu!
James Msowoya ndiye adagoletsa patadutsa mphindi makumi atatu, kenako Clever Chikwata amene anamwetsa pa mphindi 72 ndi Justice Honde yemwe adachinya pa mphindi 90 mu mphindi yachitatu yoonjezera.