Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Technology

MACRA ikuchita bwino — Suleman

Bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) lamema anthu kuti aphunzire kuyamikira bungweli chifukwa likuyesetsa kutukula njira zamakono zofalitsira uthenga komanso kuteteza aMalawi ku uthenga ndi nkhani zimene zili ndi kuthekera kobweretsa mpungwepungwe m’dziko.

Mkulu wabungweli, a Daud Suleman, wayankhula izi kutsatira pamene anthu ena akuloza zala bungweli kuti layika ndalama zochuluka pogula ndi kukhazikitsa makina atsopano ofuna kuthana ndi nkhani zabodza pamasamba a mchezo.

Kampani ya m’dziko la Ghana ndi imene yapambana kontalakiti yokhazikitsa makinawa pandalama zosachepera $1.5 miliion.

A Suleman ati bungweli lachita izi monga mwa malamulo ndipo bungweli palokha likuchita bwino kaamba lili ndi ndalama ku thumba lawo.

Iwo anati bungweli lachita phindu losachepera K13.5 billion ndipo chidwi chawo ndi chofika pomapanga K24 billion pachaka.

MACRA yatinso makinawa ndi ofunikira kwambiri pamene dziko lino likupita kuchisankho ndipo mayiko ena akhala akugwiritsa ntchito makinawa munthawi ya miliri ngati COVID-19.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

63 years for Lucy Kadzamira’s killer

MBC Online

Christian Aid donates vehicles to Ministry of Gender

MBC Online

Wanderers idzasankha mphunzitsi watsopano gawo loyamba la super league likatha

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.