Mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP), yemwenso ndi nduna ya maboma ang’ono, umodzi ndi chikhalidwe, a Richard Chimwendo Banda, ndiye wanena izi ndikulimbikitsa anthu ku Nsaru, kwa mfumu Kabudula m’boma la Lilongwe kuti apitirize kukhala pambuyo pa chipanichi ndi mtsogoleri wake, Dr Chakwera, kuti chitukuko chipitilire m’dziko muno.
Poyankhula pa msonkhano wachitukuko omwe anachititsa pabwalo la ADMARC ya Nsaru, a Chimwendo Banda anati Dr Chakwera ndi mtsogoleri yekhayo wa masomphenya yemwe akuchita zitukuko mosayang’anira chigawo chomwe anthu akuchokera.
A Chimwendo Banda ati alimi m’dziko muno, kuphatikizapo alimi afodya, akhala akugulitsa mbewu zawo pa mitengo yabwino pansi pa boma la Dr Chakwera.
Mwazina, iwo atsimikizira anthu a mderali kuti boma lipitiriza kuwapatsa thandizo la chakudya, podziwa kuti mvula sidachite bwino.
Phungu wadera lakumpoto m’boma la Lilongwe, a Monica Chang’anamuno, analimbikitsa anthu a mdelari kuti akavotere Dr Chakwera pa chisankho chapa 16 September 2025.
Iwo anayamika Dr Chakwera chifukwa cha zitukuko zimene boma lakhazikitsa mdera lawo, zomwe zasintha miyoyo ya anthu ambiri.
Wapampando wa chipanichi m’chigawo chapakati, a Patrick Zebron Chilondola, anati sakukayika kuti anthu a mdelari akavotera Prezidenti Chakwera komanso a Chang’anamuno ngati phungu wa deralo chifukwa cha chikoka chomwe alinacho.
Anthu 51,000 ndi omwe adalembetsa maina awo m’kaundula kuti adzaponye voti pa chisankho chapa 16 September 2025 mdera la kumpoto kwa boma la Lilongwe.
Pa msonkhanowu panafika nduna za boma, mafumu, akuluakulu a chipani cha MCP komanso aphungu osiyanasiyana aku nyumba ya malamulo.