Anthu ambiri ku Area 25 ku Lilongwe ndi madera ozungulira m’mawa wa lero Loweluka anasonkhana pa mlatho wa Area 49 pa msewu wopita ku Nsungwi pomwe, kwanthawi yoyamba, sitima yoyesera komanso kukonza njanji yadutsa kulowera mtunda wa Mchinji, patatha zaka makumi atatu.
Anthuwa ayamika boma kuti zimenezi zithandiza kuti katundu wambiri adziyenda mosavuta komanso kukhala wotsika mtengo.
Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, adanena pomwe ankatenga boma kuti adzaonetsetsa kuti maulendo apa njanji ayambirenso mdziko muno.
Masiku apitawa, sitima inayendanso kuchoka ku Blantyre kufika ku Lilongwe itanyamula malasha.