Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Michael Usi wati ndi okhumudwa ndi mchitidwe wa anthu ena amene akumaba thandizo la chimanga lomwe Boma likupereka kwa omwe akhudzidwa ndi njala m’dziko muno.
Dr Usi ati achita chotheka kuti m’chitidwewu uthe. Iwo ati ena omwe akuulimbikitsa ndi adindo.
Iwo anena izi pamene amatsogolera ntchito yogawa chakudya mu mzinda wa Blantyre kwa anthu okhala mu Ward ya Soche East.
Pa mwambo wina ogawa chakudyachi omwe ukuchitikira mkati mwa bwalo la Kamuzu ku Blantyre, anthu ena anapezekanso akufuna kuzembetsa chimanga, koma anawalanda asanapite patali.
Masiku awiri apitawo, Dr Usi amatsogoleranso ntchito ngati yomweyi ku Chilomoni komwe anapezanso achinyamata ena akufuna kuzembetsa chimanga.