A Abida Sidik Mia omwe ndi nduna yaza madzi ndi ukhondo komanso phungu wadera la Chikwawa Mkombezi, anakaonekela ku ofesi yachigawo chapakati ya chipani cha Malawi Congress (MCP) komwe alengeza chidwi chawo kudzaimira pa udindo wa wachiwiri kwa wachiwiri wa mtsogoleri wa chipani cha MCP pa msonkhano waukulu wa konveshoni.
Poyankhula kwa amene anafika ku ofesiyi, a Mia ati ndi wokonzeka kudzapitiriza ntchito yolimbikitsa chipani cha MCP pokonzekera chisankho cha 2025.
M’mawu ake, wapampando wachipani cha MCP mchigawo chapakati a Patrick Zebron Chilondola ati ndi wokondwa kuti nao amayi muchipanichi ali ndi chidwi chokhala mmaundindo osiyanasiyana, zomwe Prezidenti wa dziko lino amalimbikitsa.