Mayi wa pfuko lino Madam Monica Chakwera afika pa bwalo la masewero la m’boma la Rumphi komwe ali nawo pa mwambo okumbukira tsiku la anthu achialubino.
Mwazina, atafika pabwalopa, Madam Chakwera anayendera zionetsero zomwe akonza a mabungwe omwe akugwira ntchito zosiyanasiyana zothandiza anthuwa.
Nduna yoona za chisamaliro cha anthu a Jean Sendeza komanso nkulu wabungwe la United Nations m’dziko muno a Rabbacca Addah Donto komanso anthu osiyanasiyana ndi akuluakulu aboma ali nawo pamwambowu.
Patha zaka khumi tsopano kuyambira pomwe dziko la Malawi linayamba kuchita nawo chikondwererochi.