Bungwe la Malawi Agriculture and Industrial Investment Corporation (MAIIC) lapanga phindu lokwana K2.5 billion chaka chatha poyerekeza ndi K722 million mu chaka cha 2022, malinga ndi kalata yazachuma yomwe bungweli lasindikiza.
Bungweli linakhazikitsidwa ndicholinga chobwereketsa ndalama kwa alimi komanso ena amene akupanga zamafakitale.
Mkulu wogwirizira wabungweli, a Lloyd Banda, ati phinduli lakwera kamba koti abwereketsa ndalama zambiri m’chakachi.
Iwo ati chinsinsi chawo ndichoti amawunika bwino munthu kapena kampani paza kuthekera kwawo kobweza ngongole.
A Banda anawonjezera kuti m’mene ayambira chaka chino, zikuonetsa kuti apanganso phindu loposa chaka chatha.