Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Local News Nkhani

Awamanga ataba matumba 300 a chimanga cha ADMARC

Wogwira ntchito ku bungwe la ADMARC Malani Kaira wazaka 35 ndi amzake awiri: Isaac Bisayi wazaka 39 ndi Imran Mtonda wazaka 30, awamanga powaganizira kuti anazembetsa matumba 300 a chimanga cha ADMARC.

Mneneri wapolisi chigawo cha kummawa Patrick Mussa wati Bisayi ndi yemwe amayendetsa galimoto yomwe inanyamula chimangacho pomwe Ntonda ndi womuthandizira wake.

Malinga ndi a Mussa, anthuwo ananyamula matumba 600 a chimanga chomwe amachokera nacho ku Dowa kupita ku ADMARC ya Mkwepele ku Machinga.

Koma atafika pasitolo za Ntaja ku Machinga, oganiziridwawo anakhota kunyumba kwa mmodzi mwa iwo ndikutsitsa matumba 300 achimangacho.

Anthu ena omwe anaona izi, anatsina khutu apolisi omwe anamanga anthuwo ndipo apolisiwo akwanitsa kupeza matumba onse 300.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

FCB rewards civil servants

Earlene Chimoyo

A Malawi Mudzifunsa Mafunso Atsogoleri Anu Mmalo Momangodandaula — Usi

Arthur Chokhotho

CSOs hail Dr Chakwera for transparency on Reforms

Timothy Kateta
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.