Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Amipingo agwire ntchito ndi boma – Sheikh Mwalabu

Bungwe lina lomwe ndi la atsogoleri a mipingo ya chisilamu ku Lilongwe lotchedwa Muslim Community lati ndilodzipereka kugwira ntchito ndi boma popititsa patsogolo chitukuko cha dziko lino.

Poyankhula ndi atolankhani ku Lilongwe mkulu wa bungweri Sheikh Mwalabu wati mipingo ndiyofunika kwambiri pa nkhani yachitukuko.

Sheikh Mwalabu ayamikira utsogoleri wa Prezidenti  Chakwera poti waonetsera poyera kuti ndiofunira dziko lino zabwino ati poti ukugwira ntchito ndi mipingo yonse mdziko muno zomwe ati ndizofunika kwambiri pa chitukuko cha dziko.

Atsogoleriwa apemphanso nthumwi zomwe zikasankhe atsogoleri atsopano a chipani cholamula cha Malawi Congress kuti akasankhe mwanzeru makamaka atsogoleri omwe angathandizane ndi mtsogoleri wa dziko pa masomphenya ake.

Iye watinso kusapezeka kwa opikisana ndi a Chakwera pa msonkhanowu ndichitsimikizo kuti aliyense ndiokhutira ndi ulamuliro wake.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Anthu apitilira kukhuza maliro a bambo Kapusa

Blessings Kanache

NASFAM for youth involvement in agriculture

Austin Fukula

MEHA for pandemic mitigation strategies

Arthur Chokhotho
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.