Malawi Broadcasting Corporation
News Nkhani

Bushiri agawa chakudya kwa okhudzidwa ndi njala ku Nkhotakota

Prophet Shepherd Bushiri wati ndi okhudzidwa ndi mavuto anjala amene akhudza anthu ambiri okhala mdera la Sub-T/A Nkhanga m’boma la Nkhotakota.

Poyankhula pamwambo ogawa chimanga kwa anthu okwana 1,300 m’deralo, mneneri wa a Bushiri, Aubrey Kusakala anati anthu am’deralo akhale ndi chiyembekezo komanso chikhulupiliro kuti Mulungu asintha nyengo zawo.

M’mawu awo, a Group Village Headman Kakopa anati thandizoli lafika munthawi yake ndipo athokoza Prophet Bushiri chifukwa cha mtima wawo wachifundo.

Ena mwa maboma amene alandira kale chimangachi ndi monga Zomba, Lilongwe, Nsanje, Thyolo, Mulanje, Ntcheu, Karonga komanso Mangochi ndipo ntchitoyi ikupitilirabe.

 

Related posts

‘Neglecting youths undermines MW2063’

Romeo Umali

MEC impressed by progress of 3rd phase voter registration

Romeo Umali

Cultural festivals are crucial for tourism — Mzuzu City Council

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.