Malawi Broadcasting Corporation
Business Local Nkhani

Alandira mphotho ya galimoto

M’modzi mwa amayi ochita bizinesi zing’onozing’ono m’dziko muno, a Fatuma Mateyu, alandira mphotho ya galimoto ya Mitsubishi Xpander ya mtengo osachepera K60 million pamapeto a mpikisano wa Kuiphula ndi Mukuru.

Mwambowu wachitikira mumzinda wa Lilongwe ndipo poyankhulapo iwo ati mphotho ya galimotoyi yafika munthawi yake ndipo angothokoza Mulungu kuti chaka chino achiyamba ndi madalitso. “Sindimayembekezera kuti ndingapeze mphotho yotere mu mpikisano wa Mukuru, indithandiza kwambiri popititsa patsogolo mabizinesi omwe ndimachita” anatero a Mateyu omwe amaoneka odzala ndi chimwemwe.

A Fatuma Mateyu (kumanja) kulandira zikalata zaumwini wagalimoto

Mkulu oyang’anira ntchito za Mukuru m’dziko muno, a Pride Chiwaya, ati cholinga china cha mpikisanowu chinali chofuna kuphunzitsa anthu kuti adzisunga ndalama komanso kuti adzilandira ndikutumiza ndalama kudzera mu njira zovomerezeka.

A Mateyu ati amachita bizinesi yogulitsa zovala ndi zakudya zosiyanasiyana ndipo katundu wina wamalonda amam’tumiza mdziko la South Africa.

#MBCDigital
#Manthu

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mavenda ku 25 atseka sitolo ya m’mwenye kaamba kotsitsa mitengo

Mayeso Chikhadzula

Dr Chakwera urges Malawians to have hope

Eunice Ndhlovu

Akhazikitsa chipani chatsopano

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.