A Polisi ku Limbe mu mzinda wa Blantyre anjata a Paul Jalasi azaka 46, powaganizira kuti anagwilirira ana awiri a zaka zisanu ndi zitatu komanso wina wazaka zisanu zokha.
Ofalitsankhani ku Polisiyi, a Aubrey Singanyama, ati a Jalasi anawapatsa anawa mbatata kuti asakaulule pamene adachita mlanduwu ku Bangwe.
A Singanyama ati izi zidachitika pamene amayi a anawa anali kochita malonda ku msika wa Limbe ndipo m’modzi mwa amayiwa anauzidwa za upanduwu ndipo anakamang’ala nkhaniyi ku Polisi kuti bambo amene akumuganizirayu amukwidzinge.
A Jalasi amachoka m’mudzi wa Chingoni kwa mfumu yayikulu Mponda m’boma la Ntcheu.