Akatswiri pa nkhani zamalamulo a Justin Dzonzi ndi a Allan Ntata ati ntchito ikadalipo kwa amene akutsogolera chipani cha UTM, a Dalitso Kabambe, pa nkhani yawo imene ili kubwalo lamilandu.
Izi zikudza pamene bwalo lamilandu lalikulu lakana pempho la a Kabambe kuti liyimitse mlandu owaganizira kuti adagwiritsa ntchito mopanda chilolezo komanso kubisa $350 million pamene iwo adali mkulu wa Reserve Bank.
A Henry Mathanga, Cliff Chiunda komanso a Joseph Mwanamveka akukhudzidwanso ndi nkhaniyi.
M’modzi wa akatswiri a za malamulo, a Dzonzi, anati nfundo zimene a Kabambe adapititsa kubwaloli sizinali zogwira mtima.
Iwo ati mlanduwu uyenera kupitirira potsatira magawo awiri motsatira umboni umene a mbali ya boma apereke bwaloli lisadapereke chiganizo chake ngati kudzakhale koyenera kuti mlanduwu upitirire kapena ayi.
Ndipo a Ntata anati udindo uli onse wa munthu yemwe akugwira ntchito zaboma supereka chitetezo choti sungayimbidwe mlandu uliwonse monga momwe amafunira a Kabambe.
Pakadali pano, mkulu wozenga milandu kumbali ya boma, a Masauko Chamkakala, anati mboni zawo zonse ndi zokonzeka pa nkhaniyi.