Sipikala wa Nyumba ya Malamulo, a Catherine Gotani Hara, wati apereka chigamulo mawa paza mpungwepungwe umene unali m’nyumbayi akachita zokambirana ndi akuluakulu ena.
Lachinayi, a Bester Awali, omwe ndi phungu otsutsa wadera la pakati m’boma la Zomba, anaponya botolo la madzi lomwe linagwera kumbali ya Boma, zomwe zinapangitsa a Hara kunena kuti khalidweli ndi loyipa.
Izi zimachitika pamene a Joshua Malango, phungu wa pakati cha kum’mvuma kwa boma la Dedza, anapempha a Sameer Suleiman kuti achotsedwe ngati wa pampando wa komiti yoona za malimidwe kaamba ka khalidwe loyipa.
Nkhaniyi inayamba cha kum’mawa ndipo inapitilira mpaka masana, zomwe zinachititsa kuti aphungu aweruke mochedwa.
#MBCDigital
#Manthu