Malawi Broadcasting Corporation
Entertainment Nkhani

Zonke wabweranso ndi nyimbo yatsopano

Mmodzi mwa oimba nyimbo za achinyamata, Zonke Too Fresh, watulutsa kanema wa nyimbo yake yatsopano yotchedwa Vote.

Mu nyimboyi, Zonke Too Fresh, yemwe dzina lake leni leni ndi Zaithwa Mhone, akumemeza ngenge ( chiphadzuwa) kuti isankhe iye monga muja andale achitira pokopa anthu.

“Mphoto yomwe a Malawi anandipatsa kudzera mu MBC Entertainers of Year inandipatsa nyonga zapadera kuti ndipitirize kutulusa nyimbo zabwino,” watero Zonke.

Zonke Too Fresh, yemwe ali ndi zaka 22, ndiyemwe akusunga mphoto ya kanema wapamwamba mu MBC Entertainers of Year ndi nyimbo yake ya Kambuzi.

Iye amadziwikanso ndi nyimbo monga school report, pachibale pawo, mankhwala ndi mkazi wa mkalasi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

‘A Chakwera ataya kholo mu uzimu’

Beatrice Mwape

‘Boma liteteze atsikana nthawi ya ngozi zadzidzidzi’

Emmanuel Chikonso

Mudzafufuze abale anu — Zomba Mental

Simeon Boyce
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.