Sinodi ya Livingstonia mu mpingo wa CCAP, pansi pa nthambi yake ya chilungamo ndi mtendere, yati mu zipani zambiri m’dziko muno mulibemo demokalase ndi umodzi.
A Mcbowman Mulagha, mkulu wa nthambiyi, wapeleka chitsanzo chammene zinthu ziliri m’chipani cha Democratic Progressive (DPP) ndi zipani zina.
Posachedwapa, chipani cha DPP chinachotsa ena mwa atsogoleri ake kaamba kophwanya ena mwa malamulo achipanichi.
A Mulagha ati zimenezi zili ndi kuthekera koononga ndale komanso kusokoneza anthu.
“Zipani zandale m’dziko muno ziyambe kutsatira mfundo za demokalase zomwe dziko lino linayamba kutsatira zaka zambiri zapitazo, choncho tipemphe atsogoleri azipanizi kuti alore mamembala ake kupikisana m’maudindo osiyanasiyana ndikupanga zokomera amalawi,” iwo anatero.
Olemba: George Mkandawire