Chipani cha UTM chalimbikitsa achinyamata kuti alembetse mu kaundula wa unzika kuti adzakhale ndi mwai oponya nawo voti pachisankho chachikulu chomwe chichitike mdziko muno chaka cha mawa.
Mkulu wa achinyamata mu chipanichi a Penjani Kalua amalankhula izi ku Mangochi pa mwambo okweza mbendera ya chipanichi.
Chipani cha UTM akuti chinatsitsa mbendera yake mwezi wa June potsatira imfa ya mtsogoleri wake yemwenso anali wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Dr Saulos Chilima.
“Tikupempha achinyamata onse omwe akufuna kudzaponya nawo voti kuti asachite ulesi olembetsa mkaundula wa chiphaso cha unzika ngati akufuna kudzaponya nawo voti mwezi wa September chaka cha mawa,” anatero a Kalua.
Olemba: Owen Mavula