Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Tipitiriza kuthandiza Malawi – IMF

Bungwe la International Monetary Fund (IMF) lati lipitiriza kuthandiza dziko lino kuti chuma chake chipitilire kupita patsogolo.

Mkulu owona zofalitsa uthenga ku IMF, a Julie Kozack ndiwo anena izi pa msonkhano wa atolankhani wa pamakina a internet pomwe anafunsidwa kuti mkulu wa IMF, a Kristalina Georgieva anakambirana zotani ndi mtsogoleri wadziko lino, Dr. Lazarus Chakwera atakumana sabata yatha mdziko la America.

Iwo anati awiriwa anakambirana zamfundo zokweza chuma cha dziko lino, nkhani yokhuzana ndi ngongole ya ECF komanso zinthu zomwe zachitika pokhonzanso ngongole zomwe dziko lino lirinazo ndi mayiko komanso mabungwe ena.

Kenako a Kozack anati a Georgieva anatsimikizira Dr. Chakwera kuti IMF ipitiriza kuthandiza Malawi kuti chuma chipitilire kuyenda bwino.

Related posts

Additional G2G fuel trucks enter Malawi

Mayeso Chikhadzula

Twists and turns on Malawi Stock Exchange (MSE)

Romeo Umali

Chakwera wanyamuka kubwelera ku Lilongwe

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.