Nduna yoona zamphamvu zamagetsi a Ibrahim Matola yati nkofunika kuti anthu onse m’dziko muno agwirane manja popititsa patsogolo chitukuko mogwirizana ndi masomphenya a mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera.
A Matola ayankhula izi m’boma la Balaka komwe amakumana ndi mamembala azipani zosiyanasiyana zomwe zili mumgwilizano wa Tonse komanso ochita malonda.
Malinga ndi a Matola cholinga cha msonkhanowu ndi mamembala a People’s Party (PP) komanso a UTM kunali kufuna kuwafotokozela kuti amvetse bwino zomwe Dr Chakwera anayankhula m’nyumba ya malamulo potsekulira msonkhano wa aphungu.
Mwa zina a Matola anatsimikiza kuti ndi utsogoleri wa Dr Chakwera, aonetsetsa kuti vuto lakuthimathima kwa magetsi lithe ncholinga choti ntchito zamalonda zipite patsogolo.
M’mau ake mkulu wa anthu a bizinesi m’boma la Balaka, a William Kasonda, wapempha kuti ngongole za NEEF ziwafikire.
Olemba Mayeso Chikhadzula.
#mbconlineservices