Bungwe loyang’anira masewero ampira muligi yaikulu ya mdziko muno la Super League of Malawi (SULOM) ladzudzula mchitidwe omwe timu ya Mafco yachita omwe ndi otsutsana ndi malamulo ampira.
Malinga ndi chikalata chomwe bungweli latulutsa zilango ziperekedwa mogwirizana ndi zomwe zachitika m’masewero apakati pa timu ya Nyasa Big Bullets ndi Mafco FC Lamulungu pa 6 October 2024.
Chikalatachi chasonyezanso kuti SULOM yawonera kanema yemwe akuwonetsa Wongani Lungu akupondedwa ndi osewera a timu ya Mafco zomwe ati n’zokhumudwitsa komanso n’zosaloledwa m’masewero ampira wamiyendo.