Salima Sugar yati yayamba kuphunzitsa maphunziro a utsogoleri kwa anthu omwe ali ndi udindo pa kampani yawo pofuna kupititsa ntchito patsogolo.
Wapampando wa kampaniyi, a Wester Kosamu, ati zaka za m’mbuyomu pa kampaniyi pakhala pali chipwirikiti pa ntchito chifukwa ati akhala akuyendetsedwa ndi anthu ena oti analibe ukadaulo komanso mapepala owayenereza.
A Kosamu ati kupatula kusula adindowa ndikuwatumiza ku sukulu za ukachenjede, akhazikitsanso mulozo watsopano oyendetsera kampaniyi kuti izipanga phindu lochuluka ndikuonesetsa kuti Sugar wake akupezeka pa msika mosavuta komanso okwanira.