Kampani ya Salima Sugar ikupereka ndalama zokwana K498 million kwa mabanja 1,000, amene amakhala pa minda ya kampaniyi, ngati chipukuta misonzi kuti asamuke pa malowa.
Mwambo opereka ndalamazi ukuchitikira ku kampaniyi m’boma la Salima.
Mkulu oyendetsa ntchito za kampaniyi, Dr Charles Thupi, ati ndondomekoyi ndi gawo limodzi lofuna kukweza ntchito yopanga shuga ndipo malo omwe anthu amenewa amakhala ndi mbali imodzi ya minda yawo yomwe akufuna kuonjezera kulima mizimbe yochuluka kuti shuga asamasowe pa msika.
Dr Thupi ati ndalamazi ziperekedwa m’ma gawo awiri ndipo ntchito yonse ikuyembekezeka kutha m’sabata ziwiri, ndipo ndalama zokwana K250 million ndi zomwe zikuperekedwa m’gawo loyamba kwa mabanja 438.
Ambiri mwa anthuwa amagwira ntchito ku kampaniyi ndipo anagwirizana nalo ganizoli chifukwa kampaniyi inawapezera kale malo ena kunja kwa mindayi koma samachoka chifukwa anali asanalandire ndalama za chipukuta misonzi.
Izi ziri chomwechi chifukwa katundu wambiri monga mitengo ndi nyumba zikuyenera kudulidwa komanso kugwetsedwa.
Mfumu yaikulu Khombedza ya m’derali, yalangiza anthuwa kuti agwiritse bwino ntchito ndalama zomwe akulandirazi.
Iyo yayamikiranso m’gwirizano omwe ukuchitika pa nthawiyi komanso kuyamikira kampani ya Salima Sugar chifukwa cha dongosolo lawo pomwe anapereka malo ena komanso kuyikako zofunikira monga mijigo komanso zipatala, mwa zina kuti anthuwa asakavutike.
Kampani ya Salima Sugar ili pakalikiliki okonzanso ntchito zake chiyambire kuyendetsedwa ndi aMalawi.