Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Phungu apereka chipinda chogonamo atsikana pa sukulu ya Sharpevalle

Ophunzira wa Form 4 pasukulu ya Sharpevalle Community Day Secondary school ku Ntcheu, Tracy Msowoya, wati maphunziro ake tsopano ayenda bwino kutsatira Chipinda chogonamo atsikana chimene phungu waderali, Nancy Chaola Mdooko, wamanga pasukuluyi.

Msowoya akuti wakhala akukumana ndi mavuto osiyanasiyana akamayenda mtunda wokwanira ma Kilometre 9 tsiku lililonse, monga abambo ndi anyamata kumutchingira panjira ndiku mamukakamiza kuti achite nawo zibwenzi.

Wapampando wakomiti yanyumba yamalamulo ya aphungu akazi, a Rachael Zulu, wayamikira a Mdooko, amene ndi phungu wadera la Ntcheu Bwanje North komanso wachiwiri kwa nduna ya za maphunziro, kamba kachipindachi ponena kuti chithandizira kuteteza atsikana ku zinthu zosiyanasiyana komanso kuti achite bwino pamaphunziro awo.

A Mdooko amanga chipinda chogonamo atsikanachi ndi ndalama za thumba la Government to Enable Service Delivery (GESD).

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Inhouse media signs Keli P

Romeo Umali

Balaka records six cases of pink eye

Romeo Umali

Chakwera to open trade fair

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.