Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

‘Osagwiritsa ntchito ndalama za Mtukula Pakhomo ngati mkomya’

Nduna yoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo, a Jean Sendeza, alangiza amayi m’dziko muno kuti asamagwiritse ntchito ndalama za Mtukula Pakhomo kuchitira mkomya mmabanja awo koma kuti adzizigwiritsa ntchito pogula zinthu zofunikira.

Ndunayi yalangizanso atsikana kuti alimbikire sukulu osati kuthamangira kukwatiwa.

Iwo amayakhula izi m’boma la Salima kumene amayendera anthu amene akupindula ndi Mtukula Pakhomo, umene tsopano ndalama zake adzilandira kudzera palamya zammanja.

Malinga ndi a Sendeza, kulandira ndalama kudzera pa lamya kudzipereka mphamvu kwa opindula kuti adzitha kutenga ndalama mulingo umene akufuna osati zonse panthawi imodzi ngati kale.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

PODCAM urges inclusive disaster preparedness for children with disabilities

Eunice Ndhlovu

Scorchers registers first win at COSAFA

Romeo Umali

UNAIDS HAIL CHAKWERA’S ADMINISTRATION IN FIGHTING HIV/AIDS

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.