Malawi Broadcasting Corporation
Development Local News Nkhani

NRB yalemba anthu opitilira 1.5 miliyoni mu ndondomeko yakalembera

Bungwe la National Registration Bureau lati lalemba anthu 1,556,613 pa ndondomeko ya kalembera ya chiphaso cha unzika.

Mlembi wamkulu wa bungwe la National Registration Bureau, Mphatso Sambo, wati chiwerengerochi n’chachikulu poyerekeza ndi chiwerengero cha anthu 1,500,000 omwe amafuna kulembetsa.

Sambo wati bungwe lawo liyambanso kalembera wina pa 10 mwezi uno ndipo afikira madera onse adziko lino muma centre 5002, poyerekeza ndi ma centre 1250 omwe adafikira poyamba.

Sambo waonjezeranso kuti bungwe la NRB lakweza chiwerengero chosindikiza ziphaso za unzika ndipo pano akusindikiza ziphaso 15,000 pa tsiku.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Umthetho Cultural Festival gets underway

MBC Online

February registers a 58% rise in share value on MSE

Earlene Chimoyo

Let’s honour Chilima’s professional legacy – MCCCI

Earlene Chimoyo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.