Unduna woona maboma ang’ono ang’ono, umodzi komanso chikhalidwe mmawa uno ukukhazikitsa ndondomeko yachiwiri ya mphamvu ku anthu munzinda wa Lilongwe.
Mlozo wachiwiri-wu akonzamo zovuta zina zimene mlozo wakale woyamba wa 1998 unali nawo zomwe zimalepheretsa anthu kutukuka, kutenga mbali muzochitika zambiri zaboma komanso kuthandizidwa moyenera ndi makhonsolo osiyanasiyana a boma kuti mzika zikhale ndi mphamvu pochita zinthu.
Pamwambowu makhonsolo, adindo aboma, a World Banki ndi ena akhalanso ndi mwayi wophunzira momwe ndondomeko yoyamba yathandizira dziko lino kudzera mu mloza wakalewo.
Nduna yoona maboma ang’ono, a Richard Chimwendo Banda, ndiwo akhazikitse mlozo wachiwiriwu.