Mwambo oona nkhope ya muulutsi wakale pa wayilesi ya MBC, malemu Everes Kayanula, tsopano uli nkati kumudzi kwao kwa Mtsiro mfumu yaikulu Kayembe m’boma la Dowa.
Malemu Kayanula anamwalira pa 5 July mwezi uno mu nzinda wa Blantyre.
Agwira ntchito youlutsa mau kwa zaka 35 ndipo anapuma pantchito mchaka cha 2018.