Mlembi wa mkulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP), a Richard Chimwendo Banda, wachenjeza aMalawi kuti asamvere atsogoleri andale amene adayeserapo koma adakanika kutukula dziko lino.
A Chimwendo Banda amayankhula izi pa msonkano wa ndale kwa Mgona munzinda wa Lilongwe, kumene anati ntchito za boma lapano ndi zowonekeratu.
Iwo anati m’mbuyomu, aMalawi monga achigawo chakumpoto adanamizidwapo ndi boma la nthawiyo kuti liwamangira bwalo la ndege ku Mzuzu komanso sukulu ya ukachenjede ya Mombera.
A Chimwendo Banda anatinso mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, waonetsa kuti akuyika mtima pa zinthu zofunika m’dziko muno ndipo n’kofunika kuti aMalawi akhale pambuyo pake.
Olemba: Isaac Jali