Bungwe la COMSIP Cooperative Union lalimbikitsa anthu kuti adzitsatira njira za ukhondo pofuna kuti adzikhala athanzi ndi kugwira ntchito zotukula mabanja komanso madera awo.
Mkulu woyendetsa ntchito za m’chigawo cha pakati kubungweli, a Annie Nyirenda, anena izi pamene anali nawo pa ntchito yapadera yosesa ndi kuchotsa zinyalala m’misika ya Area 49 ndi 4 ways mumzinda wa Lilongwe.
Mamembala a bungweli ndi ena anakonza mwambowu mogwirizana ndi khonsolo ya mzinda wa Lilongwe, pofuna kuonetsera maphunziro okhudza za ukhondo ndi kadyedwe kabwino omwe analandira kuchokera ku COMSIP.
Poyankhula m’malo mwa khonsolo ya mzinda wa Lilongwe, a Vitumbiko Lungu, anayamikira bungwelo kaambathe kogwirana manja ndi mamembala ake pa ntchito yolimbikitsa ukhondo m’madera mwawo.