Chipani cha Malawi Congress (MCP) chati sichichita nawo ndale zoononga, zodana komanso zolozana zala ndipo m’malo mwake chipitiriza kugwira ntchito za chitukuko zolozeka zimene zitasinthe miyoyo ya anthu m’dziko muno.
Ofalitsankhani za chipanichi, a Jessie Kabwila, anena izi m’dera la T/A Masula ku Mitundu m’boma la Lilongwe kumene anakaona mmene ntchito yomanga nyumba ya atsikana achialubino a m’derali ikuyendera.
A Kabwila ati chipani chawo chikuyika pa mtima umoyo wa anthu m’dziko muno posatengera kusiyana ndipo apitiriza kukwaniritsa malonjezo amene anapereka kwa a Malawi.
Iwo ati MCP ipitiriza kugwira ntchito zachitukuko ndi kuzikwaniritsa kuti umoyo wa anthu achialubino usinthe powateteza, kuwapatsa mwayi ndi kuwathandizira m’magawo osiyanasiyana.
M’modzi mwa atsikana amene awamagira nyumba, Siyana Kamumtengo, wathokoza boma powamangira nyumbayi ndipo wati tsopano sadzikhala mwa mantha.
Boma lamanga nyumba zoposa 65 za anthuwa ndipo mwa izo, 57 zatha kale.