Bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) lati likufuna mitengo ya ma ‘smartphone’ kapena kuti lamya zammanja zomwe ziri ndi ‘internet’ zikhale zotsika mtengo mdziko muno.
Mkulu wa bungweli a Daud Suleman wati kukwera mtengo kwa lamya zammanjazi kukuchititsa kuti a Malawi ochepa okwana 1 million okha akhale ndi mwayi ogwiritsa ntchito zinthu zomwe zikupezeka pa makina atsopano a ‘internet’.
Apa iwo ati kukwera mtengoku kukuchitika chifukwa choti lamyazi amachita kuyitanitsa kuchokera mayiko akunja ndikuti zikamafika kuno zimakwera mtengo kwambiri.
“Poyesetsa kuti lamyazi zitsike mtengo tili ndi chikonzero chothandizana ndi makampani ena kuti tidziyitanitsa zipangizo zopangira malamyawa kuti tidzilumikiza konkuno ndicholinga choti mitengo itsike,” anatero a Suleman.
Wolemba: Henry Haukeya