Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Galimoto 40 zonyamula mafuta zafika m’dziko muno, zinanso 70 zifika – NOCMA

Pofuna kuonetsesa kuti mafuta a galimoto maaka diesel akupezeka m’malo onse omwetsera mafuta m’dziko muno, bungwe la National Oil Company of Malawi (NOCMA) lati galimoto 40 zonyamula mafuta tsopano zafika m’dziko muno kuchokera ku doko la Beira m’dziko la Mozambique.

Malinga ndi Mkulu ofalitsa nkhani ku bungwe la NOCMA, a Raymond Likambale, atinso panopa galimoto zina zokwana 70 zatenga kale mafuta a diesel ndipo zinyamuka ku Beira nthawi ili yonse ulendo obwera ku Malawi.

Poonjezera apo palinso sitima ina yapa mtunda yomwe yapita ku Nacala kukanyamula  diesel okwana  malita 1.6 million kuonjezera pa sitima ina yomwe yatsitsa kale malita ena 1 million  ku malo osungila mafuta ku Matindi m’boma la Blantyre,”  atero a Likambale.

Iwo ati pamene galimoto zikunyamula mafutawa ku Beira mdziko la Mozambique, zinanso zikunyamula mafuta ku Tanzania, ndipo pali chiyembekezo choti mafuta ayambanso kupezeka mosavuta masiku angapo akudzawa.

 

Olemba: Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

BALAKA POLICE INTENSIFIES FIGHT AGAINST LIVESTOCK THEFT

McDonald Chiwayula

SULOM charges Bullets with two counts of misconduct

MBC Online

World Bank yapereka $80 million ku dziko la Malawi

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.