Katakwe otchaya nkhonya, Ellen Simwaka, wati wayika chidwi chofuna kutenga lamba wa World Boxing Council (WBC) akapatsidwa mpata okumana ndi amene akufunanso lambayu.
Simwaka wayankhula izi pamene wabweleranso mu ring ndi chipambano atagonjetsa Jesca Mfinanga, wa m’dziko la Tanzania, kudzera pa ma points mu nkhonya imene inalipo usiku wapitawu ku Tanzania.
Osewerayu, amene amakhala m’dziko la South Africa, anati akumasowa masewero chifukwa osewera ena akumamuopa ndi kumukana kuti asewere naye.
“Yemwe ankasunga lambayu, Kudakwache Chiwandire, wa ku Zimbabwe adakana kusewera nane nkhonya yokonzakonza patangotsala masiku ochepa,” anadandaula Simwaka.
Padakalipano, katakwe pa zigogodoyu akusungira malamba akuluakulu awiri a WBF komanso International Boxing Federation komanso iye ali pa nambala yoyamba mu Africa mu gulu la Bantam Weight.