Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Dr Chilima anali wosayang’ana zigawo – Kaliati

Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM a Patricia Kaliati wati malemu Dr Saulos Chilima anaonetsa chitsanzo chabwino potumikira dziko lino modzipereka posayang’ana zigawo.

A Kaliati ayankhula izi ku Mzuzu pa msonkhano wokumbukira malemu Dr Chilima yemwe anali mtsogoleri wa chipani cha UTM komanso wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino.

Iwo ati Dr Chilima anaikapo mtima pofuna kusintha dziko lino komanso kuti achinyamata akhale mzika zodalirika.

Atsogoleri ena a chipani cha UTM anati chipanichi chipitilira kukhala champhamvu pofuna kukwaniritsa masomphenya a yemwe anali mtsogoleri wachipanichi Dr Saulos Chilima.

Dr Chilima pamodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu anafa pa ngozi ya ndege ku Chikangawa m’boma la Mzimba pa 10 June 2024.

Related posts

Kale Langa yagwedeza Kaning’ina

MBC Online

‘Tiganizireni poonjezera ndalama za mtukula pakhomo’

MBC Online

Nditha kusiyira sukulu panjira — Mphatso

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.