Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Saulos Chilima tsopano wafika m’dziko la Republic of Korea kumene akachite nawo msonkhano waukulu pakati pa dzikolo ndi maiko amu Africa.
Nduna yoona za ulimi, a Sam Kawale, wachiwiri kwa mlembi ku ofesi ya mtsogoleri wa dziko lino, Dr Janet Banda SC, ndi ena mwa adindo akuluakulu a boma ndi amene analindira a Chilima pamodzi ndi akazi awo a Mary Chilima pa bwalo la ndege la Incheon.
Dr Chilima akuyimira m’tsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, pa msonkhanowu omwe ukhale ukuchitika koyamba m’dziko la Korea ndipo dziko lino lili pamodzi ndi maiko makumi asanu ndi mphambu zinayi (54) amene ndi ochokera ku Africa.
Imodzi mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zimange nthenje ku mkumanowu ndi yokhudzana ndi kulimbikitsa ntchito zamalonda pakati pa dziko la Korea ndi maiko a mu Africa.
Olemba: Timothy Kateta, Seoul, Republic of Korea