Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera akukumana ndi nthumwi za mabungwe akunja amene ndi okhudzidwa ndi ngozi zomwe zinagwa mwadzidzidzi m’dziko muno.
Mkumanowu ukuchitikira ku nyumba ya boma mu mzinda wa Mzuzu.
Cholinga cha mkumanowu ndi kuthandiza boma la Malawi, kudzera ku ndondomeko ya Insurance, ku ntchito zamalimidwe m’dziko muno zomwe zakhala zikukhudzidwa ndi zotsatira za kusintha kwa nyengo.
Pa zokambiranazi, pali nduna ya zaulimi, nduna ya zachuma ndi mkulu wa nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi m’dziko muno.