Popitiriza kucheza ndi aMalawi m’madera osiyanasiyana, Prezidenti wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera masana ano acheza ndi anthu m’madera angapo munzinda wa Lilongwe.
Dr Chakwera akuchita zimenezi pofuna kuwafotokozera anthu ntchito zachitukuko zomwe boma likugwira m’madera osiyanasiyana komanso zomwe likuchita pofuna kuthandiza anthu pa mavuto awo monga njala kaamba ka ng’amba yomwe idagwa kumayambiliro a chaka chino.
Prezidenti wa dziko linoyu akumalimbikitsanso anthu kukalembetsa mukaundula wa voti pokonzekera chisankho cha chaka cha mawa.
Mwa madera ena, Dr Chakwera acheza ndi anthu ku Area 23, Kawale, Area 24, kwa Kandikole ku Area 36, kwa Chinsapo 1, Mtandile, Area 49, Area 25, pa Lilongwe TTC komanso kwa Kauma.
Pakadali pano, khwimbi lasonkhana kale pa Area 23, pomwe Dr Chakwera akuyembekezeka kufika posachedwapa.