Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Bwalo lakana pempho la Chisale

Bwalo lalikulu lomva milandu yaza chuma ku Blantyre lakana pempho la a Norman Chisale kuti lisinthe mfundo zina pa mlandu umene ukukhudza chuma chimene yemwe anali oteteza prezidenti wakaleyu ali nacho.

Mkulu oyimira boma pa mlandu ndi yemwe anatenga chiletsochi mchaka cha 2021 ndipo mwazina, chimaletsa a Chisale kugwiritsa ntchito chuma chawo china, kuphatikizapo ndalama zomwe zili kuma akaunti awo ku banki.

Boma likuzenga mlandu a Chisale kuti anapeza chuma chawo china mwachinyengo.

Aka sikoyamba kuti a Chisale akagwade ku khothi posagwrizana ndi kuletsedwa kuti asagundenso chuma chawo.

Iwo adayesera izi ku bwalo lalikulu komanso ku khothi la apilo koma zinakanika. A Chisale anati izi zimawalepheletsa kupeza ndalama zolipilira maloya omwe akuwayimira pa milandu yawo komanso kuti amavutika kupeza zinthu zina zofunika pa moyo wawo.

Komabe a khothi sanakhutire ndi madandaulo a Chisale wa.

M’chigamulo chake, Justice Anneline Kanthambi anati panalibe umboni okwanira oonetsa kuti a Chisale akuvutika popeza zinthu zofunika pa moyo wawo.

Pachifukwachi, chiletsocho chikupitilira kugwira ntchito monga malamulo okhudza milandu yopeza chuma mosadziwika bwino amanenera.  Khothi lati silidzachotsa chiletsocho ngati palibe umboni otsimikiza ndi okwanira oonetsa kuti mkuluyu akuvutikadi.

Related posts

Two jailed for vandalism and theft of Escom conductors

MBC Online

Ndege imene anakwera a Chilima yasowa

Rabson Kondowe

Youths’ agro-business mindset change is key — NEEF

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.