Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Development Local Local News Nkhani

Bungwe la SFFRFM lati zokonzekera AIP zili m’chimake

Bungwe la Small Holder Farmers Fertilizer Revolving Fund of Malawi (SFFRFM) lati zokonzekera zokhudza ntchito yogulitsa feteleza wotsika mtengo mundondomeko ya boma ya AIP zikuyenda bwino.

Wapampando wa SFFRFM, a Paul Kamlongera, ananena izi ku Blantyre pamene komiti ya nyumba ya malamulo yoona momwe mabungwe a boma akugwilira ntchito inakayendera malo amene bungweli limasungirako zipangizo zake za ulimi.

A Kamlongera anati bungwe lawo likuyetsetsa kugula feteleza ndi cholinga chakuti ikafika nthawi yogulitsa kwa alimi, zonse zikhale zili m’chimake.

Wapampando wa komitiyi, a Binton Kutsaira, anati ndi okondwa kaamba kakuti adziwonera okha m’mene zokonzekera zikuyendera ku kampani ya SFFRFM.

Iwo anati SFFRM ili ndi udindo oonetsetsa kuti ikusungira feteleza wochuluka ndi cholinga chakuti, pambali pogulitsa mu ndondomeko ya AIP, adzigulitsanso pa mtengo wa bwino kwa alimi amene sali mu ndondomekoyi pofuna kuti mitengo ya katunduyi isamakwere pa msika.

Bungwe la SFFRM ndi lomwe limakhala patsogolo pa ntchito yogulitsa zipangizo zaulimi zotsika mtengo m’dziko muno.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Nyimboyi ithandize onse osweka mitima – Sife Mw

Emmanuel Chikonso

Boma lasintha alembi ena muma unduna

Justin Mkweu

BDNC SEALS K10 MN DEAL

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.