Banki ya FDH, imene ili pa msika wa Malawi Stock Exchange, yati phindu lake la mu chaka cha 2023 likhala pakati pa K34 billion ndi K35.5 billion akachotsapo msonkho, zimene zingapindulirenso iwo amene ali ndi gawo (shares) mu bankiyi.
Banki yi yanena izi mu uthenga wake wachiwiri wa momwe yachitira pa nkhani zachuma mu chaka cha 2023.
Phinduli ndilokwera potengera ndizomwe FDH inalengeza poyamba kuti phindu la mu 2023 litha kukhala pakati pa K29.1 billion ndi K30 billion.
Phindu lomwe FDH ikuyembekezera ndilokwera ndi ma percent a pakati pa 48 ndi 55 poyelekeza ndi 2022 pomwe banki yi inapanga phindu lokwana K22.9 billion.
Poyankhulapo, m’modzi mwa anthu amene amagula masheya pa msika wa MSE a Benedicto Nkhoma ati phindu la FDH ndilosangalatsa kwa amene ali ndi masheya mu kampaneyi.
A Nkhoma ati ndizosangalatsa kuona kuti kampani za mdziko momuno zikuchita bwino ndikuthandiza dziko lino kutukuka pachuma.
Msika wa masheya wa MSE uli ndi kampani zokwana khumi, zisanu ndi imodzi ndipo zambiri ndizochokera ku gawo la mabanki.
Wolemba: Justin Mkweu