Asilikali a Malawi Defence Force agwira nzika za dziko la Ethiopia 276, za zaka za pakati pa 15 ndi 40, zimene zinazembetsedwa kuchokera m’dziko lakwawo ndipo amazisunga ku malo okhala anthu othawa kwawo ku Dzaleka m’boma la Dowa.
Asilikaliwa agwiranso atsogoleri a mchitidwe ozembetsa anthuwu asanu ndi atatu amene ndi nzikanso za dzikolo ndipo amakhala ku Dzaleka komweko.
Iwo ati mchitidwewu ndi opereka chiwopsezo ku chitetezo cha dziko lino ngakhalenso kubweretsa matenda, mwazina.
Miyezi iwiri yapitayo, asilikaliwa anagwiranso anthu ena ozembetsedwa pafupifupi 250.