Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Religion

Apostoli adzitumiza ana kusukulu ndi kuchipatala — Khonsolo ya Nkhatabay

Akhristu a Mpingo wa Seventh day Apostolic amene amakhala mmapiri akwa Changamtole ndiku Mtazi dera la Mfumu yayikulu Zilakoma ku Nkhatabay awachenjeza kuti ayambe kupita ku sukulu ndi kumapita kuchipatala ndikuti akapanda kutero awathamangitsa mdelaro.

Khonsolo ya boma la Nkhatabay ndilo lachenjeza pamene m’modzi mwa akhristuwo, amene amadziwikanso kuti a country living, a Andrea Chinyama, anayamba kuletsa ana awo pamabanja opyola 100 kupita kusukulu komanso kuletsa mabanja awo kupita ku chipatala kukalandira mankhwala ndi katemera.

Mkulu woona zosamalira anthu ku khonsoloyi, a McSence Chagomelana, anati anakhudzidwa ataona kuti ana ena asiya kupita ku sukulu chifukwa chotengera chiphunzitso cha Apositololiwo.

Ngakhale zili chomwechi, a Chinyama anatemetsa nkhwangwa pa mwala kuti sangasinthe ganizo chifukwa, “kusukulu za dziko lapansi zimati amaphunzitsa kuti munthu anachokera ku nyani pamene ife baibulo limatiuza kuti Mulungu analenga munthu mu chifanizo chake”.

Komabe, a Chagomelana mothandizana ndi mafumu aderalo apereka masiku malire pa 10 October chaka chino kuti anthuwo ayambe kutenga nawo gawo pa chitukuko posaphwanya ufulu wa ana.

Olemba: Hassan Phiri

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mia athandiza mabanja 3000 ndi chakudya ku Chikwawa

Simeon Boyce

VEEP APPLAUDS CATHOLIC CHURCH

MBC Online

PDP convention September

Emmanuel Chikonso
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.