Anthu osiyanasiyana ayamba kufika kunyumba ya wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Malemu Dr Saulos Chilima, ku Area 12 munzinda wa Lilongwe.
Ena mwa anthuwa ndi a Michael Usi omwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha UTM komanso nduna yaza chilengedwe, mamembala a chipanichi, chomwe a Chilima anali mtsogoleri wake.
Mwambo onse wa maliro ukuyembekezeka kuchitikira kunyumba yawo yaboma ku Area 12.
Ndege yomwe Dr Chilima anakwera, pamodzi ndi anthu ena asanu ndi anayi, yapezeka itagwa mu nkhalango ya Chikangawa ndipo palibe amene wapulumuka pangoziyo.