Malawi Broadcasting Corporation
Local

ALIMI A MTEDZA APINDULA

Kampani yolimbikitsa ulimi ya Pyxus International yati ifikila alimi ochuluka ndi luso lamakono lomwe lithandize kuti mtedza olimidwa mdziko muno ukhale ovomerezeka ku misika ya pa dziko lonse.

Mkulu wa kampaniyi a Peiter Sikkel anena izi atakumana ndi mtsogoleri wa dziko la Malawi, Dr Lazarus Chakwera, pambali pa mnsonkhano wa bungwe la United Nations omwe ukuchitikira mu mzinda wa New York, m’dziko la America.

Iwo ati kampani yawo yakonzeka kuthandiza alimiwa ndi mbewu ya mtedza komanso kuwapezera misika yakunja.

Kampani ya Pyxus Agriculture Limited Malawi, ikugwila kale ntchitoyi ndi ndalama zochokera ku USAID komwe alimi ayamba kale kupindula.

 

#mbcmw
#mbcnewslive
#mbconlineservices

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Gaba strikes again for Moroka

Stephen Dakalira

Court convicts two women for selling Gentamicin as HIV cure

Davie Umar

RBM MAINTAINS POLICY RATE

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.