Apolisi ya Lingadzi ku Lilongwe agwira anthu asanu ndi atatu amene akuwaganizira kuti ndi amene akhala akubera anthu pa msewu wa ABC, umene ndi ochokera kapena kupita ku Gateway Mall ndi bwalo lamasewero la Bingu.
Ofalitsankhani ku Polisi ya Lingadzi, a Cassim Manda, akuti anthuwo akhala akubera oyendetsa galimoto zinthu monga lamya za m’manja zimene amatsomphora kudzera pa zenera.
A Manda ati amene akuwaganizirawa ndi achinyamata osapyola dzaka makumi atatu.
Iwo ati ayamba kuyigwira ntchitoyi motsogozedwa ndi oyang’anira Polisiyi watsopano, a Edwin Magalasi, ndipo akwanitsa kupeza lamya zinayi zobedwa zimene ayini ake apezeka kale.