Akatswiri ovina nyimbo za Lucius Banda, Oliva Akimu komanso Isaac Nuru ati ndi osweka kamba ka imfa ya soja yemwe anali mzati pa moyo ndi luso lawo.
Poyankhula ndi MBC Digital, a Akimu ati a Banda ndi omwe anawatola ndikuwabweretsa poyera komanso kuthandizira kuti apeze maziko.
A Nuru ati anthu aphunzire kudzichepetsa monga Lucius Banda amachitira maka pothandiza kusula luso la ena.
“Apapa tikuthamangira ku Balaka kuti tikaperezeke bambo wathu Soja,” anatero onse awiri mosisima.
A Akimu ndi a Nuru akhala akuvina nyimbo za Lucius Banda kwazaka zoposa 20.