Katswiri pankhani zandale, a Undule Mwakasungula, wapempha mtsogoleri wakale wa dziko lino Professor Peter Mutharika kuti awunike mozama za zaka zawo ngati angadzakwanitse kutsogolera dziko lino moyenera.
Mu kalata yomwe a Mwakasungula atulutsa, iwo ati a Mutharika atsogoze kukonda dziko lino ndipo avomereze kuti pali zinthu zambiri zomwe boma la Tonse lakwanitsa kuzikonzanso ndikuchita potukula dziko lino.
Iwo ati potengera zaka zakubadwa, ndi zokaikitsa ngati a Mutharika angakwanitse kuyendetsa dziko lino mosadodoma.
Wolemba: Blessings Cheleuka