Nduna yoona za chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo, Dr Michael Usi, yalangiza a Malawi kuti adzitha kumafunsa mafunso atsogoleri awo mmalo momangodandaula akaona kuti zinthu sizikuyenda moyenera.
A Usi amayankhula ku Chirimba CCAP mu mzinda wa Blantyre pamene anali nawo pa mwambo wa mapemphero.
Iwo ati atsogoleri a mipingo akuyenera kulimbikitsa anthu kuti adzifunsa atsogoleri monga nduna za boma ndi aphungu, mwachitsanzo, chifukwa chimene kudera kwawo sakulandira ndalama za Mtukula Pakhomo, mwa zina.
Iwo atinso anthu adzifunsa aphungu awo momwe ndalama za chitukuko cha mmadera (CDF) azigwiritsira ntchito, poganizira kuti mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera anakweza CDF kuchoka pa K40 million kufika pa K100 million kuti chitukuko chidzioneka mmadera.
Wolemba: Arthur Chokhotho